Kunali chimwemwe chosefukira lero ku Parishi ya Mzimu Woyera – Phalula, mu Dayosezi ya Mangochi pamene a Tembo, m’modzi mwa akhristu pa parishiyi pamodzi ndi banja lawo apereka mphatso ya mtengo wapatali ya njinga yamoto ku parishiyi ndi cholinga chofuna kuchepetsa mavuto amayendedwe, amene ansembe komaso atumiki ena ampingo amakumana nawo mu parishiyi. A Tembo ndi banja lawo achita izi atamaliza ntchito yotamandika, imene ayigwira yokonzanso tchalitchi la Phalula lomwe tsopano likuoneka mokongola ndi mochititsa kaso kwambiri.
Pambuyo popereka njingayi, wapampando wa tchalitchi la Phalula, athokoza mkhristuyi kamba ka khama lake potumikira mpingo. Iwo adatiso sizitengera kukhala nazo zochuluka kuti munthu athandize mpingo koma mtima wofuna kuthandiza.
Pogwirizana ndi wapampando wa tchalitchili, Bambo Mfumu a parishiyi, Bambo Tito Bayani, ayamikira banja la a Tembo chifukwa cha ntchito zosiyanasiyana zimene amagwira pa parishiyi. M’mau awo, Bambo Bayani ati, “Nthawi yakuti akhristu azidikira kuti apangilidwa chiani ndi mpingo inatha, ino ndi nthawi yoti mkhristu aliyense azisinkhasinkha kuti ndiyichitira chiyani parishi yanga kuti ipite patsogolo.”
Gawo lalikulu la Parishi ya Phalula, imapezeka m’boma la Balaka, ndipo gawo lina locheperako, limapezeka m’boma la Neno.
Ofesi Yofalitsa Mauthenga
Dayosezi ya Mangochi

