Akhristu a Parish Ya Masuku Alandira Bambo Mfumu Awo Atsopano

Akhrisitu a parishi ya St. Ignatius Loyola – Masuku, apemphedwa kuyenda limodzi ndi ansembe awo kuti mpingo wa parishi ya Masuku upite patsogolo pa moyo wauzimu komanso wa chitukuko cha thupi. Mauwa alankhula ndi Bambo Saulos Chimbalanga, Bambo Mfumu watsopano wa parishiyi, pamwambo owalandira.

M’mau awo Bambo Francis Kachere, Bambo mthandizi wa parishiyi, apempha Akhrisitu kugwirana manja ndi Bambo Mfumu wao watsopano. Ndipo polankhulapo, wapampando wa Parishi ya Masuku, a Luka Phiri, apempha Bambo Mfumu atsopanowa kuti agwire ntchito mosamalira Akhristu osiyanasiyana, m’parishiyi; achinyamata, ana, abambo, amayi, okalamba komanso odwala, amene kawiri-kawiri amasowa Masakramenti, makamaka Sakramenti la Ukalistia.

Bambo Chimbalanga asanabwere ku Parishi ya Masuku, amatumikira ku Parishi ya St. Augustine – Mangochi Cathedral. Iwo asinthana ndi Bambo Lazarus Girevulo, amene apita ku Ulongwe, mu Ofesi ya za malamulo ampingo (Tribunal).

Bambo Saulos Chimbalanga, anadzodzedwa usembe m’chaka cha 2010. Kwao kochekera ndi ku Thyolo, m’parishi ya Thunga, koma tsopano makolo awo anakhazikika kwa Phalula, m’Dayosezi ya Mangochi.

Ofesi Yofalitsa Mauthenga – Dayosezi ya Mangochi

Leave a Comment