“Alekeni ana azibwera kwa ine, musawaletse. Paja Ufukwa wa kumwamba ndi wa anthu otere.” (Mateyu 19:14)
Pofuna kukwaniritsa mauwa, ana m’Bungwe La Utumiki wa Ana zikwizikwi, ochokera ku maparishi amu Dinale ya Mpiri, lero anali ndi mkumano wao ku Parishi ya Masuku. Mkumanowu, unayamba ndi mwambo wa Msembe ya Misa, yomwe inatsogoleledwa ndi Bambo Mfumu wa parishiyi, Bambo Saulos Chimbalanga.
Mwazina zimene anawa anachita pa mkumano waowu, ndi mpikisana wa kwizi (quiz) ya Baibulo, komanso mpikisano wa makwaya a ana (Children’s Choir Festival). Pa mipikisano yonseyi, ya kwizi komanso kwaya, ana ochokera ku Parishi ya Masuku ndiwo apambana.
M’mau awo, mkulu oyang’anira mabungwe a Papa m’Dayosezi ya Mangochi (PMS), Bambo Paul Rappozo, anati, cholinga cha mkumanowu, ndikupereka mwayi kwa ana, kudziwa za Baibulo, komanso, kuphunzitsana mayimbidwe abwino Achikatolika. Iwo anati, ndi khumbo la Ambuye Montfort Stima, Episikopi wa Dayoseziyi, kuti mpingo upereke chisamaliro chabwino kwa ana poti iwowa ndi atsogoleri amawa ampingo.
Anawa anachokera, ku maparishi onse, mu dinale ya Mpiri, kupatula, maparishi a Nsanama ndi Holy Cross. Dinale ya Mpiri inamangidwa ndi maparishi sikisi (6), omwe ndi Masuku, Holy Cross, Namandanje, St. Mary’s – Ntaja, ndi Nsanama.
Mikumanoyi ikhala ikupitirira m’madinale onse 5, amu Dayosezi ya Mangochi.
Ofesi Yofalitsa Mauthenga
Dayosezi ya Mangochi

