Episkopi wa Dayosizi ya Mangochi, Ambuye Montfort Stima, anatsogolera chinamtindi cha achinyamata ochokera ku maparishi ndi sukulu zosiyanasiyana za mu dayoseziyi pamwambo wa chaka chino wa Lamulungu lokumbukira ndi kupempherera mayitanidwe mumpingo, umene chaka chino mwambo waukulu, wachitikira ku Dayosezi ya Mangochi, m’Malawi muno. Mwambowu, unachitikira ku sukulu ya ukachenjede ya DMI – St. John the Baptist University, m’boma la Mangochi.
Mwambowu unayamba ndi mwambo wansembe ya Misa, imene anatsogolera Ambuye Montfort Stima, mothandizana ndi ansembe yosiyanasiyana amene analinawo pa mwambowu.
M’malaliko awo, Ambuye Stima alangiza achinyamata kuti akhale ochenjera pa kagwiridwe ntchito ka masamba a mchezo. “Pamene njirazi zili zamakono, komanso zothandiza pamoyo wamakono, koma pewani, kutumizirana mauthenga opanda pake”, atero Ambuye Stima.
Iwo alangiza achinyamatawa kuti, asamatanganidwe ndi zinthu zopanda pake, zomwe pambuyo pake zimawabweretsera, kapena kuwayika m’mavuto. “Ngati achinyamata mukuyenera kumadzipereka muzochitika za mumpingo, komanso kupereka nthawi yanu yochuluka kwa Mulungu”, analangiza motero Ambuye Stima. Iwo anatsindika kufunikira kwake kwakulapa ndi kutembenuka mtima, monga m’mene mtumiki Petulo anawapemphera a Yuda aja.
Ambuye Stima anati, kuti achinyamata azindikire bwino mayitanidwe awo, akuyenera kupewa makhalidwe oyipa monga chiwerewere, kumwa mowa komanso kuvala mosayera.
Ofesi Yofalitsa Mauthenga
Dayosezi ya Mangochi

