Episikopi wa Dayosezi ya Mangochi, Ambuye Montfort Stima, watsekulira sukulu ya anyamata, imene akuyitcha Limido Boy’s Catholic Primary School, m’boma la Balaka. Sukuluyi yamangidwa ndicholinga chopititsa patsogolo maphunziro a anyamata a m’mbomali.
Limido Boys Catholic Primary School, yamangidwa ndi asistere achipani cha Daughters of Wisdom, ndithandizo la ndalama lochokera kwa nzika ina yaku Italy, a Joseph Limido, atamva zamavoto amene anyamata amakumana nawo pofuna kupeza maphunziro abwino m’mbomali.
Polankhulapo, mkulu oyang’anira za maphunziro ndi masewera, m’boma la Balaka, a Saulos Namani, ati chitukukochi chabwera nthawi yabwino, poyang’anira mavuto amene anthu am’delali amakumana nawo, pankhani ya maphunziro a anyamata, ndipo sukuluyi ithandiza kwambiri pa maphunziro a anyamata.
Sukuluyi yayamba ndi ophunzira 250, amakalasi a standade 1 mpaka 6. Palichiyembekezo chakuti pomafika chaka cha mawa, sukuluyi ifika standade 7.
M’mau ake, Provincial Superior wa chipani cha Daughters of Wisdom kuno ku Malawi, Sr. Mary Chimalizeni, alankhula kuti sukuluyi ipititsa patsogolo maphunziro komanso chikhalidwe chabwino. Ndipo a Joseph Limido, amene anathandiza ndi ndalama zomangira sukuluyi, apempha ophunzira kuti adzipereke, polimbikira maphunziro awo. Ndipo m’modzi mwa ophunzira wa standade 5, Emmanuel Kalinde, wathokoza pa chiganizo chowaganizira anyamata powamangira sukuluyi. Anapitiliza kunena kuti izi zithandiza anyamata kukhala osunga mwambo, komanso olimbikira pa maphunziro.
Polankhulapo, Ambuye Montfort Stima, alimbikitsa ophunzira kukhala othokoza polimbikira maphunziro awo. Awalimbikitsa kukhala osunga mwambo. Iwo anati kuchita bwino pa maphunziro, kumayendera limodzi ndikusunga mwambo.
Ofesi Yofalitsa Mauthenga
Dayosezi ya Mangochi

