Dayosezi ya Mangochi Ipangitsa Maphunziro a Charismatic

Dayosezi ya Mangochi, kudzera mu Ofesi yoyang’anira Utumi wa Mzimu Woyera (Charismatic Movement), inakonza maphunziro apadera amamembala a bungweli. Maphunzirowa anachitikira ku St. Louis Montfort – Balaka Parish, kuyambira pa 12 April, mpaka pa 18 April 2026. Mutu waukulu wa maphunzirowa, unali “Moyo mu Uzimu” (Life in the Spirit).

Mamembala 47 ndi amene achita nawo maphunzirowa, ochekera ku ma parish a Koche, Balaka, Masuku, Mbera ndi Phalula. Amene anachititsa maphunzirowa ndi akuluakulu ochokera komiti ya pamwamba ya Utumi wa Mzimu Woyera m’Malawi muno (National Executive Committee of Charismatic Renewal Movement), motsogozedwa ndi a John Mitchell.

Pambuyo pa maphunzirowa, mthumwi zinabwereza malonje awo aubatizo, ndipo analangizidwa kuti azitsata chiphunzitso cha Mpingo ndi kugwira ntchito motsata ndondomeko ya mpingo.

Anthu amene atsata maphunzirowa adzatumidwa (commissioned) pa Lamulungu la Pentekoste ku St. Louis Montfort – Balaka Parish.

Ofesi Yofalitsa Mauthenga
Dayosezi ya Mangochi

Leave a Comment