Makwaya alimbikitsidwa kumanga umodzi pakati pawo potsanzira umodzi umene ulipo pakati pa Utatu Woyera. Mauwa alankhulidwa ndi Bambo Mfumu a Parishi ya St. Louis – Monkey-bay, Bambo Raphael Nkuzi, pamene kwaya ya Holy Rosary yochokera ku Parishi ya Likuni, mu Arkidayosezi ya Lilongwe, inakachezera kwaya inzake, ya St. Louis ya Parishi ya St. Louis – Monkey-bay.
Mau awo, wapampando wa kwaya ya Holy Rosary, a Enerst Mseuwaboma, anati cholinga cha ulendowu ndi Kudzaphunzitsana maimbidwe abwino Achikatolika, komanso kudzamanga umodzi ngati Akatolika, potengera chitsanzo cha Utatu Woyera, ngakhale akuchokera ma dayosezi osiyana. Poyankhulapo, mtsogoleri wa kwaya ya St. Louis, a Clifford Banda, athokoza kwaya ya Holy Rosary chifukwa chobwera kudzawayendera. Iwo ati kubwera kwa kwayayi kuwaphunzitsa zinthu zambiri pambali ya maimbidwe, ndipo aphunzitsa ma kwaya ena apa Parishipa, ndi maparishi ena.
Ofesi Yofalitsa Mauthenga
Dayosezi ya Mangochi

