” Ambuye zikomo, Ambuye zikomo, munandiyitana ine, mwana wanga iwe, udzakhale wansembe”, iyi ndi imodzi mwanyimbo, zambiri zimene zinamanga nthenje pamene adikoni atatu; Lucius Banda, Alfred Banda ndi Joseph Banda, amalandira Sakramenti la Ukulu loweruka pa 15 August, ku St. Louis Montfort Parish, ku Balaka. Patsikuli, ansembe ena anayi, Bambo Charles Kaponya, Clement Piluwa, Danasio Malajira, ndi Enerst Mwinganyama, amathokoza Mulungu, kuti atumikira Mulungu kwa zaka 25, ngati ansembe mu Dayosezi ya Mangochi. Mwambowu, unatsogoleledwa ndi Ambuye Montfort Stima, Episikopi wa Dayosezi ya Mangochi.
Mau awo, Ambuye Montfort Stima, anafotokoza za ulemelero wa Amayi Maria, pamene lero mpingo ukukondwerera chaka chakukwezedwa kwa Amayi Maria kumwamba. Amayi Maria, anakwezedwa kupita kumwamba chifukwa chakuvomera modzichepetsa kuyitana kwa Mulungu, kuti akhale Mayi Mpulumutsi, Ambuye Yesu Khristu. Ambuye Stima, analangiza adikoni amene amadzodzedwa unsembewa, kuti atenge Mayi Maria ngati chitsanzo chawo, ndikutengera mtima wa Amayi Maria odzichepetsa, omvera, ndikumachita kufuna kwa Mulungu.
Polanngiza ansembe amene amachita chaka chokondwerera zaka 25 ngati ansembe, Ambuye Stima anati, iwo tsopano alowa m’gulu la ansembe akuluakulu, choncho, akuyenera kupereka chitsanzo chabwino kwa Ansembe atsopanowa. “Osachimwitsa ana ang’onowa”, anatero Ambuye Stima.
Polankhula kwa makolo, Ambuye Montfort Stima anati, ngati makolo ali ndi udindo opempherera ana awo kuti agwire bwino ntchito yawo modzipereka.
Pamwambowu, panalinso, Episikopi opuma wa Dayosezi ya Mangochi, Ambuye Alessandro Pagani, ansembe, asistere, abulazala, ndi Akhristu eni ake ochokera maparishi onse, mu Dayosezi ya Mangochi, komanso kunja kwa dayosezi.
Ofesi Yofalitsa Mauthenga
Dayosezi ya Mangochi

